Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 23:18 - Buku Lopatulika

18 Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkulu, nati, Wam'nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkulu, nati, Wam'nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Iye adamtengadi mnyamatayo kupita naye kwa mkulu wa asilikali, namuuza kuti, “Mkaidi uja Paulo anandiitana, nandipempha kuti ndibwere ndi mnyamatayu kwa inu, akuti ali nanu ndi mau.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Anamutengadi mnyamatayo napita naye kwa mkulu wa asilikali uja, nati, “Wamʼndende uja Paulo anandiyitana, nandipempha kuti ndibweretse mnyamatayu kwa inu chifukwa ali ndi kanthu koti akuwuzeni.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 23:18
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndili ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anavomera, Mphunzitsi, nenani.


Ndipo khamulo ndi kapitao wamkulu, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga Iye,


Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;


Ndipo Paulo anadziitanira kenturiyo wina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkulu; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye.


Ndipo kapitao wamkulu anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Chiyani ichi uli nacho kundifotokozera?


Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m'ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwa kenturiyo dzina lake Julio, wa gulu la Augusto.


Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinachite kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma;


Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu,


Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,


koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa