Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 22:30 - Buku Lopatulika

30 Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu a milandu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Mkulu wa asilikali uja adaafuna kudziŵa kwenikweni chifukwa chimene Ayuda adaadzanenezera Paulo. Choncho m'maŵa mwake adammasula, nalamula kuti akulu a ansembe ndi onse a pa Bwalo Lalikulu lamilandu la Ayuda asonkhane. Kenaka adabwera ndi Paulo namuimika pakati pao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Mmawa mwake, mkulu wa asilikali pofuna kupeza chifukwa chenicheni chimene Ayuda amamunenera Paulo, anamumasula ndipo analamula kuti akulu a ansembe ndi onse akuluakulu a Bwalo Lalikulu asonkhane. Ndipo iye anabweretsa Paulo namuyimiritsa patsogolo pawo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 22:30
13 Mawu Ofanana  

Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;


ndipo anammanga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a mu Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu.


Pamenepo poyandikira kapitao wamkulu anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awiri; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anachita chiyani?


Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira makalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe.


Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu a milandu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.


Potero tsopano inu ndi bwalo la akulu a milandu muzindikiritse kapitao wamkulu kuti atsike naye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.


Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa kubwalo la akulu a milandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye.


Ndipo pofuna kuzindikira chifukwa chakuti anamnenera iye, ndinatsikira naye kubwalo lao la akulu a milandu.


Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anafuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.


Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang'ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndili ine, osanena nsinga izi.


Ndipo atamva ichi, analowa mu Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa a bwalo la akulu a milandu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa