Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 22:29 - Buku Lopatulika

29 Pamenepo ndipo iwo amene anati amfunsefunse, anamsiya; ndipo kapitao wamkulunso anaopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adammanga iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Pamenepo ndipo iwo amene anati amfunsefunse, anamsiya; ndipo kapitao wamkulunso anaopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adammanga iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Pompo asilikali aja amene adaati afunse Paulo mafunso, adamleka. Mkulu ujanso adachita mantha atazindikira kuti adaamanga munthu amene ali mfulu yachiroma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Iwo amene anati amufunse analeka nthawi yomweyo. Mkulu wa asilikali uja anachita mantha atazindikira kuti wamanga Paulo amene ndi nzika ya Chiroma.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 22:29
5 Mawu Ofanana  

Pamenepo poyandikira kapitao wamkulu anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awiri; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anachita chiyani?


Ndipo kapitao wamkulu anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wake waukulu. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma.


Akazi analandira akufa ao mwa kuuka kwa akufa; ndipo ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa