Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 22:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo m'mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwa kenturiyo wakuimirirako, Kodi nkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wake wosamveka?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo m'mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwa kenturiyo wakuimirirako, Kodi nkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wake wosamveka?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Pamenepo padaaimirira mtsogoleri wa gulu la asilikali 100. Tsono asilikali ake atamanga Paulo kuti amkwapule, Pauloyo adafunsa kuti, “Kodi malamulo anu amalola kukwapula mfulu yachiroma musanazenge nkomwe mlandu wake?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Atamumanga kuti amukwapule, Paulo anati kwa msilikali wolamulira asilikali 100 amene anayima pamenepo, “Kodi malamulo amalola kukwapula nzika ya Chiroma imene sinapezedwe yolakwa?”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 22:25
13 Mawu Ofanana  

Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;


Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.


Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa tsindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga.


Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya,


Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tili Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atitulutse.


Ndipo pakumva ichi kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkulu, namuuza, nanena, Nchiyani ichi uti uchite? Pakuti munthuyo ndiye Mroma.


Ndipo Paulo anadziitanira kenturiyo wina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkulu; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye.


Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikali, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma.


Koma ndinawayankha, kuti machitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho.


Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m'ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwa kenturiyo dzina lake Julio, wa gulu la Augusto.


Ndipo m'mawa mwake tinangokocheza ku Sidoni; ndipo Julio anachitira Paulo mwachikondi, namlola apite kwa abwenzi ake amchereze.


Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angachite cha uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m'nyanja, nafike pamtunda,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa