Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 22:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Apo Ambuye adandiwuza kuti, ‘Nyamuka, chifukwa Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Pamenepo Ambuye anandiwuza kuti, “Nyamuka; Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 22:21
15 Mawu Ofanana  

Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.


Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.


Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;


amene ife tinalandira naye chisomo ndi utumwi, kuti amvere chikhulupiriro anthu a mitundu yonse chifukwa cha dzina lake;


Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndili mtumwi wa anthu amitundu, ndilemekeza utumiki wanga;


kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.


koma chaonetsedwa tsopano, ndi kudziwidwa kwa anthu a mitundu yonse mwa malembo a aneneriwo, monga mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti amvere chikhulupiriro;


ndi umo anandizindikiritsa chinsinsicho mwa vumbulutso, monga ndinalemba kale mwachidule,


umene anandiika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'chikhulupiriro ndi choonadi.


umene ndaikikapo mlaliki, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa