Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 22:20 - Buku Lopatulika

20 ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kuvomerezana nao, ndi kusunga zovala za iwo amene anamupha iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kuvomerezana nao, ndi kusunga zovala za iwo amene anamupha iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Pamene ankapha Stefano, mboni yanu, inenso ndinali pomwepo. Ndinkavomerezana nawo, ndipo ndinkasunga ndine zovala za amene ankamuphawo.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Ndipo pamene ankapha Stefano, ine ndinali pomwepo kuvomereza ndi kusunga zovala za amene amamupha.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 22:20
8 Mawu Ofanana  

Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.


Chimenenso ndinachita mu Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe aakulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinavomerezapo.


Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:


ndipo anamtaya kunja kwa mzinda, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo.


Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali mu Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai.


amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.


Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu.


Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa