Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 22:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo popeza sindinapenye, chifukwa cha ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo popeza sindinapenya, chifukwa cha ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Sindidathe kupenyanso chifukwa cha kuŵala kwakukulu kuja, nchifukwa chake anzanga aja adachita kundigwira pa dzanja nkumanditsogolera mpaka kukaloŵa m'Damasiko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Anzanga anandigwira dzanja kupita nane ku Damasiko, popeza kuwala kunja kunandichititsa khungu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 22:11
4 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.


Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lake lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuunikira iwe.


Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa