Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 21:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo m'mawa mwake tinachoka, ndipo tinafika ku Kesareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo m'mawa mwake tinachoka, ndipo tinafika ku Kesareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 M'maŵa mwake tidanyamuka nkukafika ku Kesareya. Tidapita kunyumba kwa mlaliki Filipo, mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi aŵiri aja, ndipo tidakhala kunyumba kwakeko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Tinachoka mmawa mwake, mpaka tinakafika ku Kaisareya. Tinapita kukakhala mʼnyumba ya mlaliki Filipo, amene anali mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi awiri aja.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 21:8
18 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya,


Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kutulukira kunka ku Masedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.


Tsiku la Sabata tinatuluka kumuzinda kunka kumbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana.


Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake.


Ndipo pamene anakocheza pa Kesareya, anakwera naulonjera Mpingo, natsikira ku Antiokeya.


Koma ife tinatsogolera kunka kungalawa, ndipo tinapita ku Aso, pamenepo tinati timlandire Paulo; pakuti anatipangira chomwecho, koma anati ayenda pamtunda yekha.


Ndipo tinapita m'ngalawa kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Troasi; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.


Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kesareya, natenganso wina Mnasoni wa ku Kipro, wophunzira wakale, amene adzatichereza.


Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikali mazana awiri, apite kufikira Kesareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, achoke ora lachitatu la usiku;


Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m'ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwa kenturiyo dzina lake Julio, wa gulu la Augusto.


Ndipo itapita miyezi itatu tinayenda m'ngalawa ya ku Aleksandriya, idagonera nyengo ya chisanu kuchisumbuko, chizindikiro chake, Ana Amapasa.


Ndipo pamene tinalowa mu Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikali womdikira iye.


Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:


Koma m'mene abale anachidziwa, anapita naye ku Kesareya, namtumiza achokeko kunka ku Tariso.


Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;


Koma iwe, khala maso m'zonse, imva zowawa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa