Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 21:34 - Buku Lopatulika

34 Koma wina anafuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona chifukwa cha phokosolo analamulira amuke naye kulinga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Koma wina anafuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona chifukwa cha phokosolo analamulira amuke naye kulinga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Koma pakati pa anthuwo ena adayamba kufuula zina, ena zina. Chifukwa cha phokosolo mkulu wa asilikali uja sadathe kudziŵa kuti zoona zenizeni nziti. Choncho adalamula kuti amtenge Pauloyo apite naye ku linga la asilikali.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Ena mʼgulumo anafuwula chinthu china ndi enanso chinanso. Tsono popeza mkulu wa asilikaliyo sanathe kudziwa choonadi chenicheni chifukwa cha phokoso, analamula kuti Paulo atengedwe kupita ku malo a asilikali.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 21:34
8 Mawu Ofanana  

Ndipo ena anafuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwe chifukwa chake cha kusonkhana.


Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkulu, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Chigriki?


kapitao wamkulu analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake nchiyani kuti amfuulira chomwecho.


Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu a milandu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.


Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga.


Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo anamva za chifwamba chao, ndipo anadza nalowa m'linga, namfotokozera Paulo.


Koma m'mawa mwake anasiya apakavalo amperekeze, nabwera kulinga;


Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa