Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 20:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo atampangira chiwembu Ayuda, poti iye apite ndi ngalawa ku Siriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Masedoniya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo atampangira chiwembu Ayuda, poti iye apite ndi ngalawa ku Siriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Masedoniya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 nakakhalako miyezi itatu. Pamene anali pafupi kupita ku Siriya pa chombo, Ayuda adamchita chiwembu. Tsono iye adatsimikiza zodzera ku Masedoniya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kumeneko anakhala miyezi itatu. Popeza kuti Ayuda anakonza zomuchita chiwembu pamene amati azinyamuka kupita ku Siriya pa sitima ya pamadzi, iye anaganiza zobwereranso kudzera ku Makedoniya.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 20:3
19 Mawu Ofanana  

Pamenepo tinachoka ku mtsinje wa Ahava tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, kunka ku Yerusalemu; ndipo dzanja la Mulungu wathu linakhala pa ife, ndi kutilanditsa m'dzanja la mdani ndi wolalira m'njira.


Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi, tilalire osachimwa opanda chifukwa;


Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akutcha misampha; atcha khwekhwe, agwira anthu.


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mzinda wa ku Masedoniya, waukulu wa m'dzikomo, wa midzi ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena.


Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife.


Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake mu Kenkrea; pakuti adawinda.


Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.


Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya.


wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;


Ndipo m'mene atapitapita m'mbali zijazo, nawachenjeza, anadza ku Grisi.


Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kipro, tinachisiya kulamanzere, nkupita ku Siriya; ndipo tinakocheza ku Tiro; pakuti pamenepo ngalawa inafuna kutula akatundu ake.


nampempha kuti mlandu wake wa Paulo uipe, kuti amuitane iye adze ku Yerusalemu; iwo amchitira chifwamba kuti amuphe panjira.


Ndipo m'kulimbika kumene ndinafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhale nacho chisomo chachiwiri;


paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mzinda, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;


Pakutinso pakudza ife Masedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha.


Pamene ndinadza kumbali za Siriya ndi Silisiya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa