Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 20:23 - Buku Lopatulika

23 koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'mizinda yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'midzi yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Chokhachi ndikudziŵa kuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mazunzo zikundidikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Chimene ndikudziwa ndi chakuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mavuto zikundidikira.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 20:23
14 Mawu Ofanana  

pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo.


Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.


nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.


Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.


ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a mu Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu.


Pamenepo poyandikira kapitao wamkulu anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awiri; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anachita chiyani?


Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masiku asanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu.


Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike kugaleta uyu.


pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambiri ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa.


kuti asasunthike wina ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiika ife tichite izi.


Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,


ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa