Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 20:16 - Buku Lopatulika

16 Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi mu Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi m'Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Paulo anali atatsimikiza zolambalala Efeso, kuwopa kutaya nthaŵi ku dziko la Asiya. Ankafulumira kuti ngati nkotheka akakhale ali ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Paulo anali atatsimikiza kuti alambalale Efeso kuopa kutaya nthawi ku Asiya, pakuti ankafulumira kuti akafike ku Yerusalemu kuti ngati nʼkotheka kuti tsiku la Pentekosite akakhale ali ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 20:16
17 Mawu Ofanana  

Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.


Ndipo m'mene anagogoda pa chitseko cha pakhomo, anadza kudzavomera mdzakazi, dzina lake Roda.


Ndipo anapita padziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau mu Asiya;


Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.


koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.


Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena;


Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.


Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pamalo amodzi.


Koma ife tinatsogolera kunka kungalawa, ndipo tinapita ku Aso, pamenepo tinati timlandire Paulo; pakuti anatipangira chomwecho, koma anati ayenda pamtunda yekha.


Ndipo pamene anafika kuli iye, anati kwa iwo, Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthawi yonse,


Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidzandigwera ine kumeneko;


Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatere mwana wa Piro, wa ku Berea; ndipo a Atesalonika, Aristariko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Deribe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tikiko ndi Trofimo.


Ndipo tinapita m'ngalawa kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Troasi; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.


Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masiku asanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu.


Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;


Koma ndidzakhala ku Efeso kufikira Pentekoste.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa