Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 2:5 - Buku Lopatulika

5 Koma anali mu Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ochokera kumtundu uliwonse pansi pa thambo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma anali m'Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ochokera kumtundu uliwonse pansi pa thambo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono, m'Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku maiko onse a pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ayuda woopa Mulungu ochokera ku mayiko onse a dziko lapansi ankakhala mu Yerusalemu nthawi imeneyi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 2:5
17 Mawu Ofanana  

ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.


Pakuti Ine ndidziwa ntchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga.


Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,


Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.


pakuti monga mphezi ing'anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa Munthu m'tsiku lake.


Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.


Ndipo mmodzi wa iwo, dzina lake Kleopa, anayankha nati kwa Iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo mu Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano?


Koma panali Agriki ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira pachikondwerero.


ndiye munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu ndi banja lake lonse, amene anapatsa anthu zachifundo zambiri, napemphera Mulungu kosaleka.


Ndipo m'mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;


Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mzindawo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m'malire ao.


Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pamalo amodzi.


Ndipo munthu dzina lake Ananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa chilamulo, amene amchitira umboni wabwino Ayuda onse akukhalako,


Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro aakulu.


Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Etiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aetiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera;


Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.


ngatitu, mukhalabe m'chikhulupiriro, ochilimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa