Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 2:35 - Buku Lopatulika

35 kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 mpaka nditasandutsa adani ako kukhala chopondapo mapazi ako.’

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 2:35
18 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.


Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.


Okhala m'chipululu adzagwadira pamaso pake; ndi adani ake adzaluma nthaka.


Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.


Monga mwa ntchito zao momwemo Iye adzabwezera amaliwongo ake ukali, nadzabwezera adani ake chilango; nadzabwezeranso zisumbu chilango.


Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Pakuti Davide sanakwere Kumwamba ai; koma anena yekha, Ambuye anati kwa Mbuye wanga, khalani kudzanja lamanja langa,


Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.


Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.


Ndipo ndinaona chilombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo ao, osonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa