Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 2:31 - Buku Lopatulika

31 iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Khristu, kuti sanasiyidwe m'dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaone chivunde.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Khristu, kuti sanasiyidwa m'dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaona chivunde.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Ndiye kuti Davideyo adaaoneratu zimenezi, zakuti Khristu adzauka kwa akufa, ndipo pamenepo adanena mau aja akuti, “ ‘Iye sadasiyidwe ku Malo a anthu akufa, ndipo thupi lake silidaole.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Davide ataoneratu zimene zinali mʼtsogolo anayankhula za kuuka kwa Khristu, kuti Iye sanasiyidwe mʼmanda, ndipo thupi lake silinawole.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 2:31
7 Mawu Ofanana  

Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.


Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? Udzatsika kufikira ku dziko la akufa! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa mu Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.


Chifukwa anenanso mu Salimo lina, Simudzapereka Woyera wanu aone chivundi.


Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,


ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo;


Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa