Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 2:29 - Buku Lopatulika

29 Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 “Abale anga, ndingathe kulankhula nanu monenetsa za kholo lathu Davide. Iye adamwalira, naikidwa m'manda, ndipo manda ake alipo mpaka pano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 “Abale, ine ndikuwuzani motsimikiza kuti kholo lathu Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda, ndipo manda ake alipo lero lino.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 2:29
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide.


Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkulu wa dera lake lina la dziko la Betezuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi kunyumba ya amphamvu aja.


Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;


munandidziwitsa ine njira za moyo; mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu.


Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira makalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe.


Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ichi sichinachitike m'tseri.


Koma tapenyani ukulu wake wa iyeyu, amene Abrahamu, kholo lalikulu, anampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa