Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 2:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 “ ‘Mulungu akuti, Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi azidzalalika za Mulungu. Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya, ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 “ ‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse. Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, anyamata anu adzaona masomphenya, nkhalamba zanu zidzalota maloto.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 2:17
38 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anaitana ana ake aamuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo.


Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao padziko lapansi.


Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.


Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga, monga mvula yothirira dziko.


Tembenukani pamene ndikudzudzulani; taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga, ndikudziwitsani mau anga.


Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.


ndipo ulemerero wa Yehova udzavumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi, pakuti pakamwa pa Yehova panena chomwecho.


Pakuti ndidzathira madzi padziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako;


Ndipo ndidzadyetsa iwo amene atsendereza iwe ndi nyama yaoyao; ndi mwazi waowao; iwo adzaledzera monga ndi vinyo wotsekemera; anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndili Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.


Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzake, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira kulinzake, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova.


Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;


Ndipo sindidzawabisiranso nkhope yanga, popeza ndatsanulira mzimu wanga pa nyumba ya Israele, ati Ambuye Yehova.


Ndadzera tsono kukuzindikiritsa chodzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m'tsogolo.


atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.


Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.


Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.


Khalani chete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwake mopatulika.


ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.


monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha.


Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.


Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.


Koma masiku awa aneneri anatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiokeya.


Ndipo ananyamuka mmodzi wa iwo, dzina lake Agabu, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu padziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudio.


komatu ichi ndi chimene chinanenedwa ndi mneneri Yowele,


ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera.


Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.


Ndipo munthuyu anali nao ana aakazi anai, anamwali, amene ananenera.


ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.


ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.


Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.


koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;


Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.


ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa