Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 2:14 - Buku Lopatulika

14 Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu mu Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu mau anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu m'Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu mau anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Ayuda, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu kuno, tamverani ndipo mumvetsetse bwino mau anga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma Petro anayimirira pamodzi ndi atumwi khumi ndi mmodziwo ndipo anakweza mawu ake nayankhula kwa gulu la anthu nati: “Ayuda anzanga, ndi nonse amene muli mu Yerusalemu, mvetsetsani izi ndipo tcherani khutu ku zimene ndikunena.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 2:14
18 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, ngodala akusunga njira zanga.


Iwe amene utengera mau abwino ku Ziyoni, kwera iwe pamwamba paphiri lalitali; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena kumizinda ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu!


Mverani Ine, inu amene mutsata chilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang'anani kuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo.


Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kunditcherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzachokera kwa Ine, ndipo ndidzakhazikitsa chiweruziro changa chikhale kuunika kwa anthu.


Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.


Mau a alonda ako! Akweza mau, aimba pamodzi; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Yehova abwerera kudza ku Ziyoni.


Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.


Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.


Lipenga kukamwa kwako. Akudza ngati chiombankhanga, kulimbana ndi nyumba ya Yehova; chifukwa analakwira chipangano changa, napikisana nacho chilamulo changa.


Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,


Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.


Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israele, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.


Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;


nafuula, Amuna a Israele, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Agriki nalowa nao mu Kachisi, nadetsa malo ano oyera.


Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israele, kadzichenjerani nokha za anthu awa, chimene muti muwachitire.


Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye mu Mesopotamiya, asanayambe kukhala mu Harani;


Ndipo Mose, ndi ansembe Alevi ananena ndi Israele wonse, ndi kuti, Khalani chete, imvanitu, Israele; lero lino mwasanduka mtundu wa anthu wa Yehova Mulungu wanu.


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa