Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 19:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Paulo adaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda, ndipo pa miyezi itatu adakhala akulankhula molimba mtima. Ankakamba ndi anthu za ufumu wa Mulungu, nayesa kuŵakopa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Paulo analowa mʼsunagoge ndipo anayankhula molimba mtima kwa miyezi itatu, kuwatsutsa mowakopa za ufumu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 19:8
17 Mawu Ofanana  

kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;


Koma iwowa, atapita pochokera ku Perga anafika ku Antiokeya wa mu Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi.


Ndipo Paulo ndi Barnabasi analimbika mtima ponena, nati, Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.


Ndipo kunali pa Ikonio kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Agriki anakhulupirira.


Chotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m'sunagoge, ndi m'bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao.


Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.


ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.


Ndipo anafotokozera m'sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Agriki.


Ndipo anachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse akukhala mu Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Agriki.


Onsewo anali ngati amuna khumi ndi awiri.


Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawachokera, napatutsa ophunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Tirano.


Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleke usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.


Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa