Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 19:23 - Buku Lopatulika

23 Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Nthaŵi yomweyo padabuka chipolowe chachikulu chifukwa cha Njira ya Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Pa nthawi yomweyo panachitika chipolowe chachikulu chifukwa cha Njira ya Ambuye.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 19:23
10 Mawu Ofanana  

ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.


Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawachokera, napatutsa ophunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Tirano.


ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.


Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;


Koma Felikisi anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lisiasi kapitao wamkulu akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.


napempha kwa iye makalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.


paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mzinda, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;


m'mikwingwirima, m'ndende, m'maphokoso, m'mavutitso, m'madikiro, m'masalo a chakudya;


monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani tili ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa