Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 19:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawagonjetsa onsewo, kotero kuti anathawa m'nyumba amaliseche ndi olasidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti anathawa m'nyumba amaliseche ndi olasidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Kenaka munthu wogwidwa ndi mizimu yoipa uja adaŵalumphira naŵagwira onse. Adaŵagonjetsa kotero kuti iwowo adathaŵanso m'nyumba muja ali maliseche ndiponso atapwetekedwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Pamenepo munthu amene anali ndi mzimu woyipa anawalumphira nawagwira onse. Iye anawamenya kwambiri, kotero kuti anathawa mʼnyumbamo ali maliseche, akutuluka magazi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 19:16
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.


Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu.


Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa.


Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani?


Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Agriki, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu linakuzika.


Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao mu Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.


ndi kuwalonjeza ufulu, pamene iwo eni ali akapolo a chivundi; pakuti chimene munthu agonjetsedwa nacho, adzakhala kapolo wa chimenecho.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa