Machitidwe a Atumwi 19:13 - Buku Lopatulika13 Koma Ayuda enanso oyendayenda, otulutsa ziwanda, anadziyesa kutchula pa iwo amene anali ndi ziwanda dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Koma Ayuda enanso oyendayenda, otulutsa ziwanda, anadziyesa kutchula pa iwo amene anali ndi ziwanda dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Ayuda ena oyendayenda, otulutsa mizimu yoipa, nawonso adayesa kutchula dzina la Ambuye Yesu pa anthu ogwidwa ndi mizimu yoipa. Ankati, “M'dzina la Yesu amene Paulo amamlalika, ndikukulamulani kuti mutuluke.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Ayuda ena amene ankayendayenda kutulutsa mizimu yoyipa anayesa kugwiritsa ntchito dzina la Ambuye Yesu pa amene anali ndi ziwanda. Iwo popemphera amati, “Ine ndikulamulira utuluke, mʼdzina la Yesu amene Paulo amamulalikira.” Onani mutuwo |