Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:26 - Buku Lopatulika

26 ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Tsono adayamba kulankhula molimba mtima m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Koma pamene Prisila ndi Akwila anamumva, adamtenga namufotokezera Njira ya Mulungu molongosoka koposa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Iye anayamba kuyankhula mʼsunagoge molimba mtima. Pamene Prisila ndi Akula anamva, iwo anamuyitanira ku nyumba yawo ndipo anamufotokozera njira ya Mulungu molongosoka bwino.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:26
23 Mawu Ofanana  

kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira; ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;


Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.


Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake; ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira.


Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.


Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.


Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa.


Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za Iye yekha.


Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.


Chifukwa chake anakhala nthawi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anachitira umboni mau a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja ao.


Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake mu Kenkrea; pakuti adawinda.


Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;


Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.


Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye.


Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, Sindikufunani inu.


Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru.


Ngati wina ayesa kuti adziwa kanthu sanayambe kudziwa monga ayenera kudziwa.


Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,


Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa