Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:23 - Buku Lopatulika

23 Atakhala kumeneko nthawi, anachoka, napita ku madera osiyanasiyana a dziko la Galatiya ndi la Frijiya, nakhazikitsa ophunzira onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Atakhala kumeneko nthawi, anachoka, napita ku madera osiyanasiyana a dziko la Galatiya ndi la Frijiya, nakhazikitsa ophunzira onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Atakhala kumeneko kanthaŵi ndithu, adachokako nakayendera dziko la Galatiya ndi la Frijiya, akulimbikitsa ophunzira onse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Atakhala kwa kanthawi ku Antiokeya, Paulo anachokako nayendera madera onse a ku Galatiya ndi ku Frugiya kulimbikitsa ophunzira onse.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:23
22 Mawu Ofanana  

Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golide, ndi chuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wake, pamodzi ndi nsembe zaufulu.


Ndipo ine, chaka choyamba cha Dariusi Mmedi, ndinauka kumlimbikitsa ndi kumkhazikitsa.


kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe;


koma ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.


Ndipo anamuonekera Iye mngelo wa Kumwamba namlimbitsa Iye.


nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.


Ndipo Yudasi ndi Silasi, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mau ambiri, nawalimbikitsa.


Ndipo iye anapita kupyola pa Siriya ndi Silisiya, nakhazikitsa Mipingo.


Ndipo anatuluka m'ndendemo, nalowa m'nyumba ya Lidia: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.


Ndipo anapita padziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau mu Asiya;


Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena;


mu Frijiya, ndiponso mu Pamfiliya, mu Ejipito, ndi mbali za Libiya wa ku Kirene, ndi alendo ochokera ku Roma,


Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso.


ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kwa Mipingo ya ku Galatiya:


Monga tinanena kale, ndipo ndinenanso tsopano apa, ngati wina akulalikirani Uthenga Wabwino wosati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa.


ndipo chija cha m'thupi langa chakukuyesani inu simunachipeputse, kapena sichinakunyansireni, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Khristu Yesu mwini.


Koma langiza Yoswa, numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale laolao.


ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu mu Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu;


Chomwecho, tonthozanani ndi mau awa.


Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa