Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo pamene anakocheza pa Kesareya, anakwera naulonjera Mpingo, natsikira ku Antiokeya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo pamene anakocheza pa Kesareya, anakwera naulonjera Mpingo, natsikira ku Antiokeya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Pamene adafika ku Kesareya, adapita ku Yerusalemu kukacheza pang'ono ndi mpingo. Kuchokera kumeneko adapita ku Antiokeya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Pamene Paulo anafika ku Kaisareya, anakwera kukapereka moni ku mpingo kenaka anatsikira ku Antiokeya.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:22
16 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya,


Ndipo m'mawa mwake analowa mu Kesareya. Koma Kornelio analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ake ndi mabwenzi ake enieni.


Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ochokera ku Kesareya.


Ndipo kunali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnabasi, ndi Simeoni, wonenedwa Wakuda, ndi Lusio wa ku Kirene, Manaene woleredwa pamodzi ndi Herode chiwangacho, ndi Saulo.


komweko anachoka m'ngalawa kunka ku Antiokeya, kumene anaikizidwa ku chisomo cha Mulungu ku ntchito imene adaimalizayo.


Atumwi ndi abale aakulu, kwa abale a mwa amitundu a mu Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikupatsani moni:


Tsono pamene iwo anamuka anatsikira ku Antiokeya; ndipo anasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo.


Koma Paulo ndi Barnabasi anakhalabe mu Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri.


Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anachita nao.


Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikali mazana awiri, apite kufikira Kesareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, achoke ora lachitatu la usiku;


Pamenepo Fesito m'mene analowa dziko lake, ndipo atapita masiku atatu, anakwera kunka ku Yerusalemu kuchokera ku Kesareya.


Koma Fesito pofuna kuyesedwa wachisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi?


Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa