Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Iwo adakafika ku Efeso, ndipo kumeneko Paulo adasiyako Akwila ndi Prisila. Koma iye yekha adaloŵa m'nyumba yamapemphero nakambirana ndi Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Iwo anafika ku Efeso, kumene Paulo anasiyako Prisila ndi Akula. Iye yekha analowa mʼsunagoge nakambirana ndi Ayuda.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:19
21 Mawu Ofanana  

Pamene iwo anamfunsa iye kuti akhale nthawi ina yoenjezerapo, sanavomereze;


koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.


Ndipo anafika ku Efeso Myuda wina dzina lake Apolo, fuko lake la ku Aleksandriya, munthu wolankhula mwanzeru; ndipo anali wamphamvu m'malembo.


Ndipo anafotokozera m'sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Agriki.


Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena;


Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Agriki, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu linakuzika.


Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:


Ndipo pamene anamva, anadzala ndi mkwiyo, nafuula, nati, Wamkulu ndi Aritemi wa ku Efeso.


Ndipo pamene mlembi adatontholetsa khamulo, anati, Amuna a Efeso inu, munthuyu ndani wosadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo wosungira Kachisi wa Aritemi wamkulu, ndi fano lidachokera kwa Zeusi?


Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi mu Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.


Ndipo pokhala ku Mileto anatuma ku Efeso, naitana akulu a Mpingo.


Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye ku Kachisi.


Ngati ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, tidye timwe pakuti mawa timwalira.


Koma ndidzakhala ku Efeso kufikira Pentekoste.


Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali mu Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:


Monga ndinakudandaulira iwe utsalire mu Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,


(Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri mu Efeso, uzindikira iwe bwino.


Koma Tikiko ndamtuma ku Efeso.


ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.


Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba: Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa