Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:18 - Buku Lopatulika

18 Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake mu Kenkrea; pakuti adawinda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake m'Kenkrea; pakuti adawinda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Paulo adakhalabe ku Korinto masiku ambiri. Pambuyo pake adalaŵirana ndi abale, naloŵa m'chombo kupita ku Siriya pamodzi ndi Prisila ndi Akwila. Asanaloŵe m'chombomo, Paulo adameta tsitsi lake ku Kenkrea, chifukwa anali atachita lumbiro kwa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Paulo anakhalabe ku Korinto masiku ambiri. Kenaka anawasiya abale nakwera sitima ya pamadzi kupita ku Siriya, pamodzi ndi Prisila ndi Akula. Asanakakwere sitima ya pamadzi, anameta tsitsi lake ku Kenkreya chifukwa anali atalumbira.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:18
17 Mawu Ofanana  

Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wake wa kusala kwake pa khomo la chihema chokomanako, natenge tsitsi la pamutu wake wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mwamuna kapena mkazi akadzipatulira kulonjeza chowinda cha Mnaziri, kudzipatulira kwa Yehova;


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ndipo atalawirana nao, anachoka Iye, nalowa m'phiri kukapemphera.


Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),


Atumwi ndi abale aakulu, kwa abale a mwa amitundu a mu Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikupatsani moni:


Ndipo iye anapita kupyola pa Siriya ndi Silisiya, nakhazikitsa Mipingo.


Ndipo anapeza Myuda wina dzina lake Akwila, fuko lake la ku Ponto, atachoka chatsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio analamulira Ayuda onse achoke mu Roma; ndipo Paulo anadza kwa iwo:


ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.


Ndipo pamene iye anafuna kuoloka kunka ku Akaya, abale anamfulumiza, ndi kulembera makalata kwa ophunzira kuti amlandire: ndipo pamene anafika, iye anathangata ndithu iwo akukhulupirira mwa chisomo;


Chifukwa chake uchite ichi tikuuza iwe; tili nao amuna anai amene anawinda;


amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, nusunga chilamulo.


Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kipro, tinachisiya kulamanzere, nkupita ku Siriya; ndipo tinakocheza ku Tiro; pakuti pamenepo ngalawa inafuna kutula akatundu ake.


Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkrea;


Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhale ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;


Pamene ndinadza kumbali za Siriya ndi Silisiya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa