Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo anamgwira Sostene, mkulu wa sunagoge, nampanda kumpando wachiweruziro. Ndipo Galio sanasamalire zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo anamgwira Sostene, mkulu wa sunagoge, nampanda kumpando wachiweruziro. Ndipo Galio sanasamalira zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Pamenepo onsewo adagwira Sostene, mkulu wa nyumba yamapemphero ya Ayuda, nammenyera m'bwalo momwemo. Koma Galio sadasamaleko zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Kenaka iwo anagwira Sositene, mkulu wa sunagoge, ndipo anamumenya mʼbwalo la milandu momwemo. Koma Galiyo sanasamale zimenezi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:17
7 Mawu Ofanana  

akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe.


Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.


Ndipo anadzako mmodzi wa akulu a sunagoge, dzina lake Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ake, nampempha kwambiri,


Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.


Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa.


Paulo, woitanidwa akhale mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Sostene mbaleyo,


koma ife tilalikira Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu chinthu chopusa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa