Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 17:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati, Amuna inu a Atene, m'zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati, Amuna inu a Atene, m'zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Paulo adaimirira pakati pa bwalo lija la Aeropagi nati, “Inu anthu a ku Atene, pa zonse ndikuwona kuti ndinu anthu opembedza kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Paulo anayimirira mʼbwalo la Areopagi nati: “Inu anthu a ku Atene! Ine ndikuona kuti mʼnjira zonse ndinu opembedza kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 17:22
8 Mawu Ofanana  

Chilala chili pamadzi ake, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaluka ndi kufuna zoopsa.


Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Silasi ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi changu chonse, anachoka.


Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mzinda wonse wadzala ndi mafano.


Ndipo anamgwira, nanka naye ku Areopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa chiphunzitso ichi chatsopano uchinena iwe?


Koma ena anadziphatika kwa iye, nakhulupirira; mwa iwonso munali Dionizio Mwareopagi, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nao.


Ndipo pamene mlembi adatontholetsa khamulo, anati, Amuna a Efeso inu, munthuyu ndani wosadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo wosungira Kachisi wa Aritemi wamkulu, ndi fano lidachokera kwa Zeusi?


koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a chipembedzero cha iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa