Machitidwe a Atumwi 17:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Anzeru enanso a magulu a Aepikurea ndi Astoiki adadzatsutsana naye. Ena ankati, “Kodi mbutuma yolongololayi ikufunanso kunena chiyani?” Enanso ankati, “Ameneyu akukhala ngati wolalika za milungu yachilendo.” Ankanena zimenezi chifukwa iye ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Yesu, ndi za kuuka kwa akufa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Gulu la Aepikureya ndi Astoiki, anthu anzeru, anayamba kutsutsana naye. Ena a iwo anafunsa kuti, “Kodi wolongololayu akufuna kunena chiyani?” Enanso anati, “Akuoneka ngati akulalikira milungu yachilendo.” Iwo ananena zimenezi chifukwa Paulo amalalikira Uthenga Wabwino wa Yesu ndi kuuka kwa akufa. Onani mutuwo |