Machitidwe a Atumwi 17:16 - Buku Lopatulika16 Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mzinda wonse wadzala ndi mafano. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Pamene Paulo analandira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mudzi wonse wadzala ndi mafano. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Pamene Paulo ankadikira Silasi ndi Timoteo ku Atene, mtima wake udavutika kwambiri poona kuti mzinda wonse ngwodzaza ndi mafano. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Paulo akudikira Timoteyo ndi Sila ku Atene, anavutika mu mtima kwambiri poona kuti mzindawo unali odzaza ndi mafano. Onani mutuwo |