Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 17:15 - Buku Lopatulika

15 Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Silasi ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi changu chonse, anachoka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Silasi ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi changu chonse, anachoka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Anthu amene adaaperekeza Paulo aja adakafika naye mpaka ku Atene. Pambuyo pake adabwerera ku Berea, Paulo ataŵalamula kukauza Silasi ndi Timoteo kuti amlondole msanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Anthu amene anamuperekeza Paulo nafika naye ku Atene, ndipo anabwerera ku Bereya atawuzidwa kuti Sila ndi Timoteyo amutsatire msanga.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 17:15
11 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko cha amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.


Pomwepo abale anatulutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Silasi ndi Timoteo anakhalabe komweko.


Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mzinda wonse wadzala ndi mafano.


(Koma Aatene onse ndi alendo akukhalamo anakhalitsa nthawi zao, osachita kanthu kena koma kunena kapena kumva cha tsopano.)


Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati, Amuna inu a Atene, m'zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.


Zitapita izi anachoka ku Atene, nadza ku Korinto.


Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.


Chifukwa chake, posakhoza kulekereranso, tidavomereza mtima atisiye tokha ku Atene;


Pamene ndikatuma Aritema kwa iwe, kapena Tikiko, chita changu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yachisanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa