Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 17:10 - Buku Lopatulika

10 Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Silasi usiku kunka ku Berea; pamene iwo anafika komweko analowa m'sunagoge wa Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Silasi usiku kunka ku Berea; pamene iwo anafika komweko analowa m'sunagoge wa Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Kutangoda, abale aja adapititsa Paulo ndi Silasi ku Berea. Atafika kumeneko, adakaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mdima utagwa, abale anatumiza Paulo ndi Sila ku Bereya. Atafika kumeneko anapita ku sunagoge ya Ayuda.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 17:10
16 Mawu Ofanana  

Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),


Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:


Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda.


Ndipo Paulo, monga amachita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m'malembo, natanthauzira,


Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Silasi; ndi Agriki akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi aakulu osati owerengeka.


Pamene sanawapeze anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akulu a mzinda, nafuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;


Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatere mwana wa Piro, wa ku Berea; ndipo a Atesalonika, Aristariko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Deribe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tikiko ndi Trofimo.


Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.


koma ophunzira ake anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa mu dengu.


koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.


Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumzinda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa