Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 16:27 - Buku Lopatulika

27 Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Woyang'anira ndende uja atadzuka, naona kuti zitseko zonse za ndende nzotsekuka, adaayesa kuti akaidi athaŵa. Pamenepo adasolola lupanga lake nati adziphe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Woyangʼanira ndende uja atadzuka ku tulo, anaona kuti zitseko za ndende zinali zotsekula, ndipo anasolola lupanga lake nafuna kudzipha chifukwa ankaganiza kuti amʼndende athawa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 16:27
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.


Kunali tsono, pakuona Zimiri kuti nkhondo yalowa m'mzinda, anakwera pa nsanja ya nyumba ya mfumu, nadzitenthera ndi moto nyumba ya mfumu, nafa;


Ndipo iye anataya pansi ndalamazo pa Kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi.


Ndipo pamene Herode adamfunafuna, wosampeza, anafunsitsa odikira nalamulira aphedwe. Ndipo anatsika ku Yudeya kunka ku Kesareya, nakhalabe kumeneko.


Koma Paulo anafuula ndi mau aakulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tili muno.


Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere.


Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa