Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 16:23 - Buku Lopatulika

23 Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m'ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m'ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Ataŵakwapula kwambiri, adaŵaponya m'ndende, nalamula woyang'anira ndendeyo kuti aŵasunge bwino, angathaŵe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Atawakwapula kwambiri anawaponya mʼndende, nalamula woyangʼanira kuti awasunge mosamalitsa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 16:23
21 Mawu Ofanana  

Koma wompereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona ndiyeyo, mumgwire Iye.


Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.


Koma kutacha, panali phokoso lalikulu mwa asilikali, Petro wamuka kuti.


Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska.


Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa.


Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere.


nathira manja atumwi, nawaika m'ndende ya anthu wamba.


nanena, Nyumba yandende tinapeza chitsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense.


Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.


napempha kwa iye makalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.


Kodi ali atumiki a Khristu? (Ndilankhula monga moyaluka), makamaka ine; m'zivutinso mochulukira, m'ndende mochulukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawirikawiri.


m'mikwingwirima, m'ndende, m'maphokoso, m'mavutitso, m'madikiro, m'masalo a chakudya;


Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu,


Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,


m'menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mau a Mulungu samangika.


koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu;


Pamenepo Yoswa analamulira ansembe, ndi kuti, Kwerani kutuluka mu Yordani.


Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu.


Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa