Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 16:13 - Buku Lopatulika

13 Tsiku la Sabata tinatuluka kumuzinda kunka kumbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Tsiku la Sabata tinatuluka kumudzi kunka kumbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Pa tsiku la Sabata tidatuluka mumzindamo kupita kumtsinje kumene tinkaganiza kuti kuli malo opemphererako. Tsono tidakhala pansi nkumalankhula ndi akazi amene adaasonkhana kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Pa tsiku la Sabata tinatuluka mu mzindawo kupita ku mtsinje kumene timayembekezera kukapeza malo opempherera. Tinakhala pansi ndipo tinayamba kuyankhula ndi amayi amene anasonkhana pamenepo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 16:13
17 Mawu Ofanana  

Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye analowa m'ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pamtunda.


Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.


Ndipo analikuphunzitsa m'sunagoge mwina, tsiku la Sabata.


Koma mamawa anadzanso ku Kachisi, ndipo anthu onse anadza kwa Iye; ndipo m'mene anakhala pansi anawaphunzitsa.


Koma iwowa, atapita pochokera ku Perga anafika ku Antiokeya wa mu Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi.


Ndipo pakutuluka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo.


Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake.


Ndipo anapita padziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau mu Asiya;


Ndipo Paulo, monga amachita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m'malembo, natanthauzira,


Ndipo anafotokozera m'sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Agriki.


Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.


Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,


Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.


Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.


ngatitu, mukhalabe m'chikhulupiriro, ochilimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa