Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 16:12 - Buku Lopatulika

12 pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mzinda wa ku Masedoniya, waukulu wa m'dzikomo, wa midzi ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mudzi wa ku Masedoniya, waukulu wa m'dzikomo, wa milaga ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Kuchokera kumeneko tidapita ku Filipi, mzinda wa m'chigawo choyamba cha m'dera lija la Masedoniya, ndiponso boma la Aroma. Tidakhala mu mzinda umenewo masiku angapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kuchokera kumeneko tinapita ku Filipi, boma la Aroma ndiponso mzinda waukulu wa dera la Makedoniya. Tinakhala kumeneko masiku owerengeka.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 16:12
14 Mawu Ofanana  

Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kutulukira kunka ku Masedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.


ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuichita, ndife Aroma.


Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife.


Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.


Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.


Ndipo m'mzinda monse munachita piringupiringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, alendo anzake a Paulo.


Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya.


Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo atampangira chiwembu Ayuda, poti iye apite ndi ngalawa ku Siriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Masedoniya.


Ndipo tinapita m'ngalawa kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Troasi; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.


Ndipo m'mene tidalowa m'ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe.


Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.


Paulo ndi Timoteo, akapolo a Yesu Khristu, kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:


chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;


koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa