Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 15:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Atakambirana nthaŵi yaitali, Petro adaimirira naŵauza kuti, “Abale anga, mukudziŵa kuti pa masiku oyamba aja Mulungu adandisankha ine pakati pa inu kuti ndilalike Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina, kuti amve ndi kukhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Atakambirana kwambiri Petro anayimirira, ndipo anawayankhula nati: “Abale, mukudziwa kuti masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu kuti anthu a mitundu ina amve kuchokera pakamwa panga mawu a Uthenga Wabwino ndi kukhulupirira.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 15:7
25 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.


Ndipo Yehova anatulutsa dzanja lake, nakhudza pakamwa panga; nati Yehova kwa ine, Taona ndaika mau anga m'kamwa mwako;


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.


Yohane anayankha nati, Munthu sangathe kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kuchokera Kumwamba.


Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.


Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikira mitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,


Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.


Komatu tauka, nutsike, ndipo upite nao, wosakayikakayika; pakuti ndawatuma ndine.


Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.


Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.


Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.


Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake; ndipo Barnabasi anatenga Marko, nalowa m'ngalawa, nanka ku Kipro.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kesareya, natenganso wina Mnasoni wa ku Kipro, wophunzira wakale, amene adzatichereza.


Koma zimene Mulungu analalikiratu m'kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Khristu, Iye anakwaniritsa chotero.


amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davide mtumiki wanu, mudati, Amitundu anasokosera chifukwa chiyani? Nalingirira zopanda pake anthu?


Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;


Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa