Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 15:24 - Buku Lopatulika

24 Popeza tamva kuti ena amene anatuluka mwa ife anakuvutani ndi mau, nasocheretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulire;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Popeza tamva kuti ena amene anatuluka mwa ife anakuvutani ndi mau, nasocheretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulira;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Tamva kuti anthu ena ochokera m'gulu lathu akhala akukuvutani ndi kukusokonezani maganizo. Amenewo sitidaŵatume ndife ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Ife tamva kuti anthu ena ochokera pakati pathu, amene sitinawatume anakusokonezani maganizo ndi kukuvutitsani ndi zimene amakuwuzani.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 15:24
12 Mawu Ofanana  

Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zachabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.


Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapanda kudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.


umene suli wina; koma pali ena akuvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Khristu.


Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakuvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza chitsutso chake.


Mwenzi atadzidula, iwo akugwedezetsani inu.


Mulibe kanthu ndi Khristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo.


Uwakumbutse izi, ndi kuwachitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asachite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.


Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa