Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 15:22 - Buku Lopatulika

22 Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Pamenepo atumwi ndi akulu a mpingo, pamodzi ndi mpingo wonse, adavomerezana kusankha anthu ena pakati pao kuti aŵatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Barnabasi. Adasankha Yudasi, wotchedwa Barsabasi, ndiponso Silasi, anthu aulemu pakati pa abale,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Pamenepo atumwi ndi akulu ampingo, pamodzi ndi mpingo onse, anagwirizana zosankha anthu ena pakati pawo kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Bamaba. Iwo anasankha Yudasi, wotchedwa Barsaba ndi Sila, anthu awiri amene anali atsogoleri pakati pa abale,

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 15:22
29 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse.


Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kuchita chowauza mfumu ndi akulu mwa mau a Yehova.


Ndipo chinthuchi chinayenera m'maso mwa mfumu ndi msonkhano wonse.


Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wotchedwa Barsabasi, amene anatchedwanso Yusto, ndi Matiasi.


Pamenepo iwotu, akubalalika chifukwa cha chisautsocho chidadza pa Stefano, anafikira ku Fenisiya, ndi Kipro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha.


Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kipro, ndi Kirene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Agriki, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.


Ndipo mbiri yao inamveka m'makutu a Mpingo wakukhala mu Yerusalemu; ndipo anatuma Barnabasi apite kufikira ku Antiokeya;


Koma masiku awa aneneri anatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiokeya.


Atumwi ndi abale aakulu, kwa abale a mwa amitundu a mu Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikupatsani moni:


chinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Barnabasi ndi Paulo,


Tatumiza tsono Yudasi ndi Silasi, omwenso adzakuuzani ndi mau zinthu zomwezo.


Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko cha amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.


Tsono pamene iwo anamuka anatsikira ku Antiokeya; ndipo anasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo.


Ndipo Yudasi ndi Silasi, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mau ambiri, nawalimbikitsa.


Koma Paulo anasankha Silasi, namuka, woikizidwa ndi abale ku chisomo cha Ambuye.


Koma pamene ambuye ake anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Silasi, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akulu,


Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;


Ndipo mdindo anaitanitsa nyali, natumphira m'kati, alinkunthunthumira ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Silasi,


Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Silasi usiku kunka ku Berea; pamene iwo anafika komweko analowa m'sunagoge wa Ayuda.


Pomwepo abale anatulutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Silasi ndi Timoteo anakhalabe komweko.


Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Silasi; ndi Agriki akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi aakulu osati owerengeka.


Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.


Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;


Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silivano ndi Timoteo) sanakhale eya ndi iai, koma anakhala eya mwa Iye.


Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu: Chisomo kwa inu ndi mtendere.


Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu:


Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa