Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 15:14 - Buku Lopatulika

14 Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Simoni wafotokoza za m'mene Mulungu pachiyambi pomwe adakumbukira anthu a mitundu ina, pa kupatula ena pakati pao kuti akhale anthu akeake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Simoni watifotokozera mmene Mulungu poyamba paja anaonetsa kukhudzidwa kwake pomwe anatenga anthu a mitundu ina kukhala ake.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 15:14
11 Mawu Ofanana  

anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.


Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.


chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu wathu. M'menemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife.


Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.


amene ife tinalandira naye chisomo ndi utumwi, kuti amvere chikhulupiriro anthu a mitundu yonse chifukwa cha dzina lake;


Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.


Simoni Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m'chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa