Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 15:10 - Buku Lopatulika

10 Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la ophunzira goli, limene sanathe kunyamula kapena makolo athu kapena ife?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la ophunzira goli, limene sanatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono mukumuyeseranji Mulungu pakuika m'khosi mwa ophunzirawo goli limene ngakhale makolo athu kapena ife tomwe tidalephera kulisenza?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Tsopano, chifukwa chiyani mukuyesa Mulungu poyika goli mʼkhosi la ophunzira, limene ngakhale ife kapena makolo athu sangathe kulisenza?

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 15:10
11 Mawu Ofanana  

Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe. Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?


Koma Ahazi anati, Sindipemphai ngakhale kumyesa Yehova.


Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chao.


Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.


Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe.


koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?


Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.


chimene makolo anu anandiyesa nacho, ndi kundivomereza, naona ntchito zanga zaka makumi anai.


ndicho chiphiphiritso cha kunthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbumtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa