Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 14:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo pa Listara panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwake, wopunduka chibadwire, amene sanayende nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo pa Listara panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwake, wopunduka chibadwire, amene sanayenda nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ku Listara kunali munthu wina wopunduka miyendo amene ankangokhala pansi. Adaabadwa wolumala ndipo chikhalire chake sadayende.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ku Lusitra kunali munthu wolumala miyendo, amene sanayendepo chibadwire chake.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 14:8
9 Mawu Ofanana  

Wodwalayo anayankha, Ambuye, ndilibe wondiviika ine m'thamanda, paliponse madzi avundulidwa; koma m'mene ndilinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine.


Pamene analalikira Uthenga Wabwino mumzindamo, nayesa ambiri ophunzira, anabwera ku Listara ndi Ikonio ndi Antiokeya,


iwo anamva, nathawira kumizinda ya Likaoniya, Listara ndi Deribe, ndi dziko lozungulirapo:


Ndipo anafikanso ku Deribe ndi Listara; ndipo taonani, panali wophunzira wina pamenepo, dzina lake Timoteo, amake ndiye Myuda wokhulupirira; koma atate wake ndiye Mgriki.


Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa mu Kachisi;


ngati ife lero tiweruzidwa chifukwa cha ntchito yabwino ya pa munthu wodwala, ndi machiritsidwe ake,


mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa