Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 14:6 - Buku Lopatulika

6 iwo anamva, nathawira kumizinda ya Likaoniya, Listara ndi Deribe, ndi dziko lozungulirapo:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 iwo anamva, nathawira kumidzi ya Likaoniya, Listara ndi Deribe, ndi dziko lozungulirapo:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Atumwi aja atamva zimenezi, adathaŵira ku Listara ndi ku Deribe, mizinda ya ku Likaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Koma atazindikira zimenezi, anathawira ku Lusitra ndi Derbe, mizinda ya ku Lukaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo,

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 14:6
12 Mawu Ofanana  

Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.


Pamene makamu anaona chimene anachita Paulo, anakweza mau ao, nati m'chinenero cha Likaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu.


Ndipo pa Listara panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwake, wopunduka chibadwire, amene sanayende nthawi zonse.


Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m'mizinda yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.


Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatere mwana wa Piro, wa ku Berea; ndipo a Atesalonika, Aristariko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Deribe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tikiko ndi Trofimo.


koma chiwembu chao chinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;


mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa