Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 14:20 - Buku Lopatulika

20 Koma pamene anamzinga ophunzirawo, anauka iye, nalowa m'mzinda; m'mawa mwake anatuluka ndi Barnabasi kunka ku Deribe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Koma pamene anamzinga ophunzirawo, anauka iye, nalowa m'mudzi; m'mawa mwake anatuluka ndi Barnabasi kunka ku Deribe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Koma ophunzira ena atasonkhana nkumzungulira, iye adauka naloŵanso mumzindamo. M'maŵa mwake iye ndi Barnabasi adapita ku Deribe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Koma ophunzira atamuzungulira, Pauloyo anayimirira nalowanso mu mzindawo. Mmawa mwake iye ndi Barnaba anachoka ndi kupita ku Derbe.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 14:20
13 Mawu Ofanana  

ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti chaka chonse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.


Ndipo ophunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala mu Yudeya;


Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina.


nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.


Ndipo anakhala pamenepo ndi ophunzira nthawi yaikulu.


iwo anamva, nathawira kumizinda ya Likaoniya, Listara ndi Deribe, ndi dziko lozungulirapo:


Ndipo anafikanso ku Deribe ndi Listara; ndipo taonani, panali wophunzira wina pamenepo, dzina lake Timoteo, amake ndiye Myuda wokhulupirira; koma atate wake ndiye Mgriki.


Ndipo anatuluka m'ndendemo, nalowa m'nyumba ya Lidia: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.


Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya.


monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani tili ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa