Machitidwe a Atumwi 14:13 - Buku Lopatulika13 Koma wansembe wa Zeusi wa kumaso kwa mzinda, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Koma wansembe wa Zeusi wa kumaso kwa mudzi, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Nyumba yopembedzeramo Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo. Tsono wansembe wake adabwera ku zipata atatenga ng'ombe yozekedwa maluŵa m'khosi. Iyeyo pamodzi ndi anthu onse aja adaafuna kudzapereka nsembe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Wansembe wa Zeusi amene nyumba yopembedzera Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo, anabweretsa ngʼombe yayimuna yovekedwa nkhata za maluwa pa chipata cha mzindawo chifukwa iyeyo pamodzi ndi anthu ena onse aja amafuna kudzipereka nsembe kwa Paulo ndi Barnaba. Onani mutuwo |