Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:31 - Buku Lopatulika

31 ndipo anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 ndipo anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 ndipo pa masiku ambiri adakhala akuwonekera kwa anthu aja amene adaamperekeza ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya. Amenewo ndiwo amene akumchitira umboni kwa anthu tsopano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa amene anayenda naye kuchokera ku Galileya mpaka ku Yerusalemu. Iwowa tsopano ndi mboni zake kwa anthu a Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:31
18 Mawu Ofanana  

Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira.


Inu ndinu mboni za izi.


Ndipo inunso muchita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira chiyambi.


amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.


kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife.


kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;


Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.


Ndipo ife ndife mboni za zonse adazichita m'dziko la Ayuda ndi mu Yerusalemu; amenenso anamupha, nampachika pamtengo.


si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.


Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse.


ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ichi ife tili mboni.


Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa