Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m'chipululu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m'chipululu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 adaŵasamalabe mopirira m'chipululu zaka makumi anai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ndipo Iye anapirira khalidwe lawo mʼchipululu kwa zaka makumi anayi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:18
19 Mawu Ofanana  

Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvere; chifukwa chake munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko.


Ndipo khamu lonse la ana a Israele linadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu;


Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.


popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;


Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro mu Ejipito, ndi mu Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai.


ndi kuchipululu, kumene munapenya kuti Yehova Mulungu wanu anakunyamulani, monga anyamula mwana wake wamwamuna, m'njira monse munayendamo, kufikira mutalowa m'malo muno.


Kumbukirani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m'chipululu; kuyambira tsikuli munatuluka m'dziko la Ejipito, kufikira munalowa m'malo muno munapikisana ndi Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa