Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:14 - Buku Lopatulika

14 Koma iwowa, atapita pochokera ku Perga anafika ku Antiokeya wa mu Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Koma iwowa, atapita pochokera ku Perga anafika ku Antiokeya wa m'Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Kuchokera ku Perga iwo adapitirira nakafika ku Antiokeya m'dera la Pisidiya. Pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapempherero ya Ayuda, nakhala pansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Kuchokera ku Perga anapita ku Pisidiya wa ku Antiokeya. Pa tsiku la Sabata analowa mʼsunagoge, nakhala pansi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:14
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.


Ndipo pakutuluka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo.


Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mzinda wonse kumva mau a Mulungu.


Ndipo Paulo ndi Barnabasi analimbika mtima ponena, nati, Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.


Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.


Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mzinda; namuyesa kuti wafa.


Tsiku la Sabata tinatuluka kumuzinda kunka kumbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana.


Ndipo Paulo, monga amachita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m'malembo, natanthauzira,


Ndipo anafotokozera m'sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Agriki.


Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.


Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.


mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa