Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 12:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo tsiku lopangira Herode anavala zovala zachifumu, nakhala pa mpando wachifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo tsiku lopangira Herode anavala zovala zachifumu, nakhala pa mpando wachifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Adapangana tsiku, ndipo pa tsikulo Herode adavala zovala zake zachifumu nkukhala pa mpando wake wachifumu, nayamba kuŵalankhula anthu aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Pa tsiku limene anasankha Herode, atavala zovala zake zaufumu, anakhala pa mpando wake ndipo anayankhula kwa anthuwo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 12:21
10 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zao zachifumu pabwalo popondera mphesa pa khomo la chipata cha Samariya; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao.


M'makutu mwake mumveka zoopsetsa; pali mtendere amfikira wakumuononga.


Mtima wa munthu unyada asanaonongeke; koma chifatso chitsogolera ulemu.


Ndipo manda akuza chilakolako chake, natsegula kukamwa kwake kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo.


Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.


Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.


Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu.


Ndipo anthu osonkhanidwawo anafuula, Ndiwo mau a Mulungu, si a munthu ai.


Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Ananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.


M'mawa mwake tsono, atafika Agripa ndi Berenise ndi chifumu chachikulu, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitao aakulu, ndi amuna omveka a mzindawo, ndipo pakulamulira Fesito, anadza naye Paulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa